Psalms 137:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lilime langa likangamire ku mnakanaka m'kamwa mwanga, ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu ndi kukuwona kuti ndiwe wondisangalatsa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lilime langa limamatike kunsaya zanga, ndikapanda kukumbukira inu; ndikapanda kusankha Yerusalemu koposa chimwemwe changa chopambana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu, ngati sindiyesa iwe chimwemwe changa chachikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lilime langa limamatike ku nsaya zanga, Ndikapanda kukumbukila inu; Ndikapanda kusankha Yerusalemu Koposa cimwemwe canga copambana.