Psalms 137:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumbukirani, Inu Chauta, zimene adachita Aedomu pa tsiku lija la kuwonongeka kwa Yerusalemu, muja ankati, “Mgwetseni pansi, mgwetseni pansi, mpaka pa maziko ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita pa tsiku limene Yerusalemu anagonja. Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi mpaka pa maziko ake!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, kumbukilani ana a Edomu Tsiku la Yerusalemu; Amene adati, Gamulani, gamulani, Kufikira maziko ace.