Psalms 138:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzagwada kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera ndipo ndidzayamika dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu ndi kukhulupirika kwanu, pakuti Inu mwakuza dzina lanu ndi mawu anu kupambana zinthu zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzagwadira kuloza ku Kacisi wanu woyera, Ndi kuyamika dzina lanu, Cifukwa ca cifundo canu ndi coonadi canu; Popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.