Psalms 14:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumtima mwake munthu wopusa amati, “Kulibe Mulungu.” Anthu otereŵa ndi oipa, amachita zonyansa, palibe ndi mmodzi yemwe wochita zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; Salimo la Davide. Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Chitsiru chimati mu mtima mwake, “Kulibe Mulungu.” Oterewa ndi oyipa ndipo ntchito zawo ndi zonyansa; palibe amene amachita zabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Waucitsiru amati mumtima mwace, Kulibe Mulungu. Acita zobvunda, acita nchito zonyansa; Kulibe wakucita bwino.