Psalms 14:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chibwere ndithu chipulumutso cha Israele kuchokera ku Ziyoni. Chauta akadzaŵabwezera ufulu anthu ake, Yakobe adzakondwera, Israele adzasangalala kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga, pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndithu, chipulumutso cha Israeli chidzachokera ku Ziyoni! Pamene Yehova abwezeretsa ufulu wa anthu ake, Yakobo akondwere ndipo Israeli asangalale!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwenzi cipulumutso ca Israyeli citacokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ace a m'nsinga, Pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israyeli.