Psalms 141:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musalole kuti mtima wanga upendekere ku zoipa, ndisadzipereke ku ntchito zoipa pamodzi ndi anthu ochita zoipa, ndisadye nawo maphwando ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mtima wanga usalinge kuchinthu choipa, kuchita ntchito zoipa ndi anthu akuchita zopanda pake; ndipo ndisadye zankhuli zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musalole kuti mtima wanga ukokedwere ku zoyipa; kuchita ntchito zonyansa pamodzi ndi anthu amene amachita zoyipa; musalole kuti ndidye nawo zokoma zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mtima wanga usalinge ku cinthu coipa, Kucita nchito zoipa Ndi anthu akucita zopanda pace; Ndipo ndisadye zankhuli zao.