Psalms 141:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wolungama angathe kundimenya kapena kundidzudzula chifukwa andimvera chifundo, koma ndisalandire ulemu kwa anthu oipa, pakuti ndimapemphera motsutsana ndi ntchito zao zoipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu wolungama andikanthe, chimenecho ndiye chifundo; andidzudzule ndiye mafuta pa mutu wanga. Mutu wanga sudzakana zimenezi. Komabe pemphero langa nthawi zonse ndi lotsutsana ndi ntchito za anthu ochita zoyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akandipanda munthu wolungama ndidzati ncifundo: Akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; Mutu wanga usakane: Pakuti pangakhale posautsidwa iwo ndidzawapempherera.