Psalms 142:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mtima wanga ufooka, Inu mumadziŵa zoti ndichite. Adani anditchera msampha m'njira imene ndimayendamo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo ananditchera msampha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mzimu wanga walefuka mʼkati mwanga, ndinu amene mudziwa njira yanga. Mʼnjira imene ndimayendamo anthu anditchera msampha mobisa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamene mzimu wanga unakomoka m'kati mwanga, munadziwa njira yanga. M'njira ndiyendamo anandichera msampha,