Psalms 143:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani pemphero langa, Inu Chauta. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Mundiyankhe chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndi kulungama kwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Salimo la Davide. Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga; ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Salimo la Davide. Yehova imvani pemphero langa, mvetserani kulira kwanga kopempha chifundo; mwa kukhulupirika kwanu ndi chilungamo chanu bwerani kudzandithandiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Imvani pemphero langa, Yehova; ndicherere khutu kupemba kwanga; Ndiyankheni mwa cikhulupiriko canu, mwa cilungamo canu.