Psalms 144:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana athu aamuna pachinyamata pao akhale amphamvu ngati mitengo, ana athu aakazi akhale okongola ngati nsanamira zozokotedwa zapangodya, zoti zikometse nyumba yaufumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuti ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; ana athu akazi ngati nsanamira za kungodya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ana aamuna pa chinyamata chawo adzakhala ngati mbewu yosamalidwa bwino, ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zosemedwa bwino, zokongoletsera nyumba yaufumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuti ana athu amuna akhale ngati mmera udakula usanakhwime; Ana athu akazi ngati nsanamira za kungondya, zosema zikometsere nyumba ya mfumu.