Psalms 15:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi amene sasinjirira ndipo sachita anzake zoipa, kapena kumafalitsa mbiri yoipa ya anzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo mʼkamwa mwake simutuluka mawu osinjirira, amene sachitira choyipa mnansi wake kapena kufalitsa mbiri yoyipa ya munthu mnzake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amene sasinjirira ndi lilime lace, Sacitira mnzace coipa, Ndipo satola msece pa mnansi wace.