Psalms 15:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi amene amanyoza munthu womkana Mulungu, koma amalemekeza anthu omvera Chauta. Ndi amene amachitadi zimene walonjeza, ngakhale zikhale zoŵaŵa chotani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
amene sapereka ulemu kwa munthu woyipa. Koma amalemekeza amene amaopa Yehova, amene amakwaniritsa zomwe walonjeza ngakhale pamene zikumupweteka,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'maso mwace munthu woonongeka anyozeka; Koma awacitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lace, sasintha ai.