Psalms 17:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, ndi dzanja lanu mundilanditse kwa adani, kwa anthu amene moyo wao umangosamala zapansipano. Muŵalange ndi zoŵaŵa zimene mudaŵasungira. Nawonso ana awo akhale nazo zambiri, ndipo iwowo asiyireko ana aonso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova, pulumutseni ndi dzanja lanu kwa anthu otere, kwa anthu a dziko lino amene mphotho yawo ili mʼmoyo uno. Inu mumaletsa njala kwa amene asangalatsidwa nanu; ana awo aamuna ali ndi zinthu zambiri, ndipo iwo amasunga chuma cha ana awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, Kwa anthu a dziko lapansi pano amene colowa cao ciri m'moyo uno, Ndipo mimba yao muidzaza ndi cuma canu cobisika: Akhuta mtima ndi ana, Nasiyira ana amakanda zocuruka zao.