Psalms 18:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; mau anga anawamva m'Kachisi mwake, ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m'makutu mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinalirira kwa Mulungu wanga kuti andithandize. Ali mʼNyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika pamaso pake ndi mʼmakutu mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'kusauka kwanga ndinaitana Yehova, Ndipo ndinakuwira Mulungu wanga; Mau anga anawamva m'Kacisi mwace, Ndipo mkuwo wanga wa pankhope pace unalowa m'makutu mwace.