Psalms 18:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo dziko lapansi lidanjenjemera ndi kuchita chivomezi. Maziko a mapiri nawonso adanjenjemera ndi kugwedezeka, chifukwa Iye adaakalipa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, ndipo maziko a mapiri anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi. Ndi maziko a mapiri ananjenjemera Nagwedezeka, pakuti anakwiya iyeyo.