Psalms 18:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'mphuno mwake munkafuka utsi, m'kamwa mwake munkatuluka moto woononga, makala amoto anali laŵilaŵi kuchokera m'kamwa momwemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Unakwera utsi woturuka m'mphuno mwace: Ndi moto wa m'kamwa mwace unanyeka: Nuyakitsa makara.