Psalms 2:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumgonjere molapa, kuwopa kuti angakukwiyireni, ndipo inu mungaonongeke, chifukwa ukali wake umayaka msanga. Ngodala onse amene amathaŵira kwa Iye.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira, Ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wace. Odala onse akumkhulupirira Iye.