Psalms 20:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho tifuule ndi chimwemwe chifukwa chakuti mwapambana pa nkhondo, tikweze mbendera kutamanda dzina la Mulungu wathu. Chauta akupatse zonse zimene wapempha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tidzafuula mokondwera mwa chipulumutso chanu, ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera; Yehova akwaniritse mapempho ako onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu, Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tidzapfuula mokondwera mwa cipulumutso canu, Ndipo m'dzina la Mulungu wathu tidzakweza mbendera: Yehova akwaniritse mapempho ako onse.