Psalms 21:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu ikusangalala chifukwa mwaipatsa mphamvu, Inu Chauta, ikukondwa kwambiri chifukwa mwaipambanitsa ndinu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu, chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu; Adzakondwera kwakukuru m'cipulumutso canu!