Psalms 22:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji? Chifukwa chiyani simukundithandiza mpang'ono pomwe, chifukwa chiyani simukumva mau a kubuula kwanga?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kwa Mkulu wa Nyimbo; pa Ajelet Hasakara. Salimo la Davide. Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa chipulumutso changa, ndi kwa mau a kubuula kwanga?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa “Mbawala yayikazi ya Mmawa.” Salimo la Davide. Mulungu wanga, Mulungu wanga, nʼchifukwa chiyani mwandisiya? Chifuwa chiyani simukundithandiza ndi pangʼono pomwe? Nʼchifukwa chiyani simukumva mawu a kudandaula kwanga?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine? Mukhaliranji kutali kwa cipulumutso canga, ndi kwa mau a kubuula kwanga?