Psalms 22:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kukhosi kwanga kwauma ngati phale, lilime langa lakangamira ku nsagwada. Inu mwandisiya pa fumbi kuti ndifere pomwepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mphamvu yanga yauma ngati phale; ndi lilime langa likangamira kunsaya zanga; ndipo mwandifikitsa kufumbi la imfa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mphamvu zanga zauma ngati phale, ndipo lilime langa lamamatira ku nsagwada; mwandigoneka mʼfumbi la imfa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mphamvu yanga yauma ngati phale; Ndi lilime langa likangamira ku nsaya zanga; Ndipo mwandifikitsa ku pfumbi la imfa.