Psalms 22:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pakuti sadanyoze munthu wozunzika, sadaipidwe ndi masautso ake, sadamubisire nkhope yake, koma adamumvera pamene adamdandaulira.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwe ndi zunzo la wozunzika; ndipo sanambisire nkhope yake; koma pomfuulira Iye, anamva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Iye sanapeputse kapena kunyoza kuvutika kwa wosautsidwayo; Iye sanabise nkhope yake kwa iye. Koma anamvera kulira kwake kofuna thandizo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti sanapeputsa ndipo sananyansidwa ndi zunzo la wozunzika; Ndipo sanambisira nkhope yace; Koma pompfuulira Iye, anamva.