Psalms 22:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukulu, zowinda zanga ndidzazichita pamaso pa iwo akumuopa Iye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Ndidzakwaniritsa lonjezo langa pamaso pa amene amaopa Inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Lemekezo langa lidzakhala la Inu mu msonkhano waukuru: Zowinda zanga ndidzazicita pamaso pa iwo akumuopa Iye.