Psalms 22:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu onse odzitama adzamuŵeramira. Anthu onse oloŵa m'manda nawonso adzamugwadira, ndiye kuti onse osatha kudzisungira moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira; onse akutsikira kufumbi adzawerama pamaso pake, ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu olemera onse a dziko lapansi adzachita phwando ndi kulambira; onse amene amapita ku fumbi adzagwada pamaso pake; iwo amene sangathe kudzisunga okha ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onenepa onse a pa dziko lapansi adzadya nadzagwadira: Onse akutsikira kupfumbi adzawerama pamaso pace, Ndi iye amene sadziwa kusunga moyo wace.