Psalms 22:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komabe Inu ndinu amene mudalola kuti ndibadwe. Inu ndinu chikhulupiriro changa, mudandilera bwino ndili mwana woyamwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa; wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe Inu ndinu amene munandibadwitsa, munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga. Munachititsa kuti ndizikudalirani ngakhale pa nthawi imene ndinkayamwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Inu ndinu wondibadwitsa: Wondikhulupiritsa pokhala ine pa bere la mai wanga.