Psalms 23:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inde, ndingakhale ndiyenda m'chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale ndiyende mʼchigwa cha mdima wakuda bii, sindidzaopa choyipa, pakuti Inu muli ndi ine; chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditonthoza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inde, ndingakhale ndiyenda m'cigwa ca mthunzi wa Imfa, Sindidzaopa coipa; pakuti Inu muli ndi ine: Cibonga canu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine,