Psalms 25:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa cha dzina lanu, Yehova, ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova, khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa ca dzina lanu, Yehova, Ndikhululukireni kusakaza kwanga, pakuti ndiko kwakukuru.