Psalms 25:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuika mtima wanga pa Inu Mulungu wanga. Musalole kuti adani anga andichititse manyazi, musalole kuti akondwere pamene ine ndikuvutika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, ndisachite manyazi; adani anga asandiseke ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndimadalira Inu Mulungu wanga. Musalole kuti ndichite manyazi kapena kuti adani anga andipambane.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, Ndisacite manyazi; Adani anga asandiseke ine.