Psalms 25:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musakumbukile zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu: Mundikumbukile monga mwa cifundo canu, Cifukwa ca ubwino wanu, Yehova.