Psalms 27:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kachisi wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cinthu cimodzi ndinacipempha kwa Yehova, ndidzacilondola ici: Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, Kupenya kukongola kwace kwa Yehova ndi kufunsitsa m'Kacisi wace.