Psalms 27:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa m'tsenjezi mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti pa tsiku la msautso Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo; adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa kuti pa dzuwa la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwace: Adzandibisa m'tsenjezi mwa cihema cace; Pathanthwe adzandikweza.