Psalms 27:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzapambana adani anga ondizungulira, ndipo ndidzapereka nsembe m'Nyumba mwake ndili kufuula ndi chimwemwe. Ndidzaimba nyimbo yotamanda Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; ndipo ndidzapereka m'chihema mwake nsembe za kufuula mokondwera; ndidzaimba, inde, ndidzaimbira Yehova zomlemekeza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero mutu wanga udzakwezedwa kuposa adani anga amene andizungulira; pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe; ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano mutu wanga udzakwezeka pamwamba pa adani anga akundizinga; Ndipo ndidzapereka m'cihema mwace nsembe za kupfuula mokondwera; Ndidzayimba, inde, ndidzayimbira Yehova zomlemekeza.