Psalms 27:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musandibisire nkhope yanu. Musandipirikitse ine mtumiki wanu mokwiya, Inu amene mwakhala mukundithandiza. Musanditaye, musandisiye ndekha, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musandibisire ine nkhope yanu; musachotse kapolo wanu ndi kukwiya. Inu munakhala thandizo langa; musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa chipulumutso changa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musandibisire nkhope yanu, musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo; mwakhala muli thandizo langa. Musandikane kapena kunditaya, Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musandibisire ine nkhope yanu; Musacotse kapolo wanu ndi kukwiya: Inu munakhala thandizo langa; Musanditaye, ndipo musandisiye Mulungu wa cipulumutso canga,