Psalms 28:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikuitana Inu Chauta, Inu thanthwe langa, musachite ngati simukundimva, chifukwa ngati mukhala chete, ndidzafanafana ndi anthu otsikira ku manda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Salimo la Davide. Kwa Inu, Yehova, ndidzafuulira; thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva; pakuti ngati munditontholera ine, ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Salimo la Davide. Kwa Inu ine ndiyitana, Yehova ndinu Thanthwe langa; musakhale osamva kwa ine. Pakuti mukapitirira kukhala chete, ndidzakhala ngati iwo amene atsikira ku dzenje.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kwa Inu, Yehova, ndidzapfuulira; Thanthwe langa, musandikhalire ngati wosamva: Pakuti ngati munditontholera ine, Ndidzafanana nao iwo akutsikira kumanda.