Psalms 28:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musandichotsere kumodzi ndi anthu oipa, anthu amene amachita zonyenga, amene amalankhula zamtendere ndi anzao, koma mitima yao ndi yodzaza ndi chidani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musandikokere kutali pamodzi ndi anthu oyipa, pamodzi ndi iwo amene amachita zoyipa, amene amayankhula mwachikondi ndi anzawo koma akusunga chiwembu mʼmitima mwawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musandikoke kundicotsa pamodzi ndi oipa, Ndi ocita zopanda pace; Amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, Koma mumtima mwao muli coipa.