Psalms 28:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muŵabwezere anthu otere molingana ndi ntchito zao, muŵalange molingana ndi zoipa zimene ankachita. Muŵabwezere molingana ndi ntchito zao, Muŵalange molingana ndi kuipa kwa ntchito zao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muwapatse monga mwa ntchito zao, ndi monga mwa choipa chochita iwo; muwapatse monga mwa machitidwe a manja ao; muwabwezere zoyenera iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muwabwezere chifukwa cha zochita zawo ndi ntchito zawo zoyipa; abwezereni chifuwa cha zimene manja awo achita ndipo mubweretse pa iwo zimene zowayenera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muwapatse monga mwa nchito zao, ndi monga mwa coipa cocita iwo: Muwapatse monga mwa macitidwe a manja ao; Muwabwezere zoyenera iwo.