Psalms 28:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi chikopa changa; mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza, chifukwa chake mtima wanga ukondwera kwakukulu; ndipo ndidzamyamika nayo nyimbo yanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi chishango changa; mtima wanga umadalira Iye, ndipo Ine ndathandizidwa. Mtima wanga umalumphalumpha chifukwa cha chimwemwe ndipo ndidzayamika Iye mʼnyimbo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova ndiye mphamvu yanga, ndi cikopa canga; Mtima wanga wakhulupirira Iye, ndipo anandithandiza: Cifukwa cace mtima wanga ukondwera kwakukuru; Ndipo ndidzamyamika nayo Nyimbo yanga.