Psalms 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, dzambatukani, mundipulumutse Inu Mulungu wanga. Adani anga onse mwaŵaomba makofi, anthu oipa mwaŵagulula mano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; mwawathyola mano oipawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzukani, Inu Yehova! Pulumutseni, Inu Mulungu wanga. Akantheni adani anga onse pa msagwada; gululani mano a anthu oyipa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ukani Yehova; ndipulumutseni, Mulungu wanga! Pakuti mwapanda adani anga onse patsaya; Mwawatyola mano oipawo.