Psalms 30:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa. Simudalole kuti adani anga akondwere poona kuti ndikuvutika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Salimo la Davide. Nyimbo yakuperekera nyumba kwa Mulungu. Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa, ndipo simunandikondwetsera adani anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu. Ndidzakukwezani Yehova, chifukwa mwanditulutsa kwakuya, ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa, Ndipo simunandikondwetsera adani anga,