Psalms 30:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse; utha kuchezera kulira usiku wonse, koma chimwemwe chimabwera mmawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mkwiyo wace ukhala kanthawi kokha; Koma kuyanja kwace moyo wonse: Kulira kucezera, Koma mamawa kuli kupfuula kukondwera.