Psalms 30:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kodi mudzapindulanji pa imfa yanga ngati nditsikira ku manda? Kodi ine nditasanduka fumbi, ndingathe kukutamandani? Kodi pamenepo ndingathe kulalika za kukhulupirika kwanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje? Ngati fumbi lidzayamika Inu? Ngati lidzalalikira choonadi chanu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga ngati nditsikira ku dzenje? Kodi fumbi lidzakutamandani Inu? Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwazi mwanga muli phindu lanji, potsikira ine kudzenje? Ngati pfumbi lidzayamika Inu? ngati lidzalalikira coonadi canu?