Psalms 31:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Moyo wanga ukutha chifukwa cha chisoni, zaka zanganso zikutha chifukwa cha kulira kwambiri. Mphamvu zanga zatheratu chifukwa cha kulakwa kwanga, mafupa anga agooka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti moyo wanga watha ndi chisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo. Mphamvu yanga yafooka chifukwa cha kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula; mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso, ndipo mafupa anga akulefuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti moyo wanga watha ndi cisoni, ndi zaka zanga zatha ndi kuusa moyo: Mphamvu yanga yafoka cifukwa ca kusakaza kwanga, ndi mafupa anga apuwala.