Psalms 31:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adani anga onse amandinyodola, anzanga omwe amandiyesa chinthu chonyansa. Anthu odziŵana nawo amandiyesa chinthu choopsa. Anthu ondiwona mu mseu amandithaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndakhala chotonza chifukwa cha akundisautsa onse, inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa choopsa; iwo akundipenya pabwalo anandithawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha adani anga onse, ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga; ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga. Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndakhala cotonza cifukwa ca akundisautsa onse, Inde, koposa kwa anansi anga; ndipo anzanga andiyesa coopsa: Iwo akundipenya pabwalo anandithawa.