Psalms 31:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa, kuwateteza ku ziwembu za anthu; mʼmalo anu okhalamo mumawateteza kwa anthu owatsutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa ciwembu ca munthu: Mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.