Psalms 31:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mundikomere mtima, Inu Chauta, pakuti ndili m'zovuta. Maso anga atupa chifukwa cha chisoni. Mumtima mwanga ndi m'thupi momwe mwadzaza zovuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mundichitire chifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine. Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mavuto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto; maso anga akulefuka ndi chisoni, mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mundicitire cifundo, Yehova, pakuti ndasautsika ine: Diso langa, mzimu wanga, ndi mimba yanga, zapuwala ndi mabvuto,