Psalms 32:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zisoni zambiri zigwera woipa; koma chifundo chidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zowawa ndi zambiri za anthu oyipa koma chikondi chosatha cha Yehova chimamuzinga munthu amene amadalira Iye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zisoni zambiri zigwera woipa: Koma cifundo cidzamzinga iye wakukhulupirira Yehova.