Psalms 32:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ndidavomera tchimo langa kwa Inu, sindidabise kuipa kwanga. Ndidati, “Ndidzaulula machimo anga kwa Chauta,” pomwepo Inu mudakhululukiradi mlandu wa machimo anga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova machimo anga; ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero ine ndinavomereza tchimo langa kwa Inu, sindinabise mphulupulu zanga. Ndinati, “Ine ndidzawulula zolakwa zanga kwa Yehova, ndipo Inu munandikhululukira mlandu wa machimo anga.” Sela
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinabvomera coipa canga kwa Inu; Ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. Ndinati, Ndidzaululira Yehova macimo anga; Ndipo munakhululukira coipa ca kulakwa kwanga.