Psalms 35:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzasangalala ndi mtima wonse ndi kunena kuti. “Ndani angafanefane ndi Inu Chauta, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka kwa munthu wopambana pa mphamvu, Inu amene mumapulumutsa munthu wofooka ndi wosoŵa kwa munthu wolanda zinthu zake?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Thupi langa lidzafuwula mokondwera, “Ndani angafanane nanu Yehova? Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri, osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, Wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, Ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?