Psalms 35:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
monga ngati ndikuchitira chisoni bwenzi langa kapena mbale wanga. Ndinkayenda khumakhuma ngati munthu wolira maliro a mai wake, nditaŵerama ndi kumalira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndakhala ine monga ngati iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga; polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndinayendayenda ndi kulira maliro, kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga. Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima kukhala ngati ndikulira amayi anga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndakhala ine monga ngad iye anali bwenzi langa, kapena mbale wanga: Polira ndinaweramira pansi, monga munthu wakulira maliro amai wace.