Psalms 35:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Chauta, mudzakhala mpaka liti mukungoyang'ana? Landitseni kwa anthu ofuna kundiwononga, mupulumutse moyo wanga ku mikangoyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye, mudzapenyererabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, wanga wa wokha kwa misona ya mkango.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana? Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo, moyo wanga wopambana ku mikango.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye, mudzapenyerabe nthawi yanji? Bwezani moyo wanga kwa zakundiononga zao, Wanga wa wokha kwa misona ya mkango.